audio
audioduration (s)
1.12
18.5
raw_text
stringlengths
1
297
normalized_text
stringlengths
1
267
gender
stringclasses
16 values
Akuluakulu a nthambi yoona za misewu akuchita zokambirana ndi ma Kampani okonza misewu kuti apeze nzeru pa momwe angachitire kuti ntchito yokonza misewu m'dziko muno ifulumire
Akuluakulu a nthambi yoona za misewu akuchita zokambirana ndi ma Kampani okonza misewu kuti apeze nzeru pa momwe angachitire kuti ntchito yokonza misewu m'dziko muno ifulumire
Female
Wapampando wa nthambiyi a Matilda Matabwa wati ntchito zokonza misewu zikuchedwa kwambiri
Wapampando wa nthambiyi a Matilida Matabwa wati ntchito zokonza misewu zikuchedwa kwambiri
Female
zomwe zikupangitsa anthu kudandaula ndi matope m'misewu komanso kuloza chala nthambiyi kuti ikulephera ntchito
zomwe zikupangitsa anthu kudandaula ndi matope m'misewu komanso kuloza chala nthambiyi kuti ikulephera ntchito
Female
A Matabwa, ati n'zokhumudwitsa kuti ntchito yokonza misewu m'mizinda ndi m'maboma zikuchedwa, ndipo ati n'zokhumudwitsa kwambiri kuona ntchito m'malo ena zitaimiratu
A Matabwa, ati n'zokhumudwitsa kuti ntchito yokonza misewu m'mizinda ndi m'maboma zikuchedwa, ndipo ati n'zokhumudwitsa kwambiri kuona ntchito m'malo ena zitaimiratu
Female
Mmodzi wa okonza misewu Engineer Rocky Kaunda wati Kampani zokonza misewu sizikupatsidwa malo ogwilira ntchito abwino ndipo izi ndi zomwe zikuchititsa ntchitozi kuchedwa
Mmodzi wa okonza misewu Injiniya Roke Kaunda wati Kampani zokonza misewu sizikupatsidwa malo ogwilira ntchito abwino ndipo izi ndi zomwe zikuchititsa ntchitozi kuchedwa
Female
Mwa zina, a Kaunda ati iwo akufuna mitengo ya ma kontilakiti awo ikwere kutsatira kugwa kwa ndalama ya Kwacha
Mwa zina, a Kaunda ati iwo akufuna mitengo ya ma kontilakiti awo ikwere kutsatira kugwa kwa ndalama ya Kwacha
Female
Anthu okhala ku dera la Mbedza ku Zomba ati salola kuti anthu ena amange nyumba mu Phiri la Chipalanje kaamba koti malowa ndi otetezedwa
Anthu okhala ku dera la Mbedza ku Zomba ati salola kuti anthu ena amange nyumba mu Phiri la Chipalanje kaamba koti malowa ndi otetezedwa
Female
M'malo mwake, anthuwa abzala mitengo yomwe Mfumu yaikulu Mulumbe yati iwonesetsa kuti yatetezedwa
M'malo mwake, anthuwa abzala mitengo yomwe Mfumu yaikulu Mulumbe yati iwonesetsa kuti yatetezedwa
Female
Khansala wa derali, a Steven Bamusi, wati iwo ndi anthu achidwi ndipo awonesetsa kuti atsatira zomwe Mfumuyi yanena
Khansala wa derali, a Steven Bamusi, wati iwo ndi anthu achidwi ndipo awonesetsa kuti atsatira zomwe Mfumuyi yanena
Female
Asilikali aku Cobbe Barracks nawo adakhamukira ku phirilo kuti likatenge nawo gawo
Asilikali aku kobe Balakisi nawo adakhamukira ku phirilo kuti likatenge nawo gawo
Female
M'mawu ake, mkulu wa asilikali ku Cobbe Barracks, Lieutenant Colonel Peter Overton Ng'oma
M'mawu ake, mkulu wa asilikali ku Kobe balakisi, Lutenantu kolonelo pita ovatoni Ng'oma
Female
anati iwo akuyenera kukhala patsogolo pa nkhani yoteteza chilengedwe kaamba koti amagwilira ntchito zawo mu thengo
anati iwo akuyenera kukhala patsogolo pa nkhani yoteteza chilengedwe kaamba koti amagwilira ntchito zawo mu thengo
Female
A polisi m'boma la Kasungu amanga mlangizi wa pa chipatala cha Nkhamenya mishoni, a Ishmael Chisemphere, a zaka 35, powaganizira kuti adagwilira mtsikana wa zaka 10
A polisi m'boma la Kasungu amanga mlangizi wa pa chipatala cha Nkhamenya mishoni, a Ishumaeli Chisemphere, a zaka fete faifi, powaganizira kuti adagwilira mtsikana wa zaka 10
Female
Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za polisi m'bomali, a Miracle Mkozi, wati izi zidachitika pa 19 January chaka chino, m'dera la Mchenga
Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za polisi m'bomali, a Milako Mkozi, wati izi zidachitika pa naintini Januwale chaka chino, m'dera la Mchenga
Female
Patsikuli, a Chisemphere adapita kukamwa mowa pa malo ena ku Mchenga, ndipo ali mkati momwa mowawu, anadatengera mtsikanayu m'nyumba momwe adagonana naye, atero a Mkozi
Patsikuli, a Chisemphere adapita kukamwa mowa pa malo ena ku Mchenga, ndipo ali mkati momwa mowawu, anadatengera mtsikanayu m'nyumba momwe adagonana naye, atero a Mkozi
Female
Apolisi yaying'ono ya Nkhamenya atamva za nkhaniyi adatengera mtsikanayu ku chipatala kuti akamuyeze, ndipo zotsatira za chipatala zidaonetsa kuti mtsikanayu adagonedwadi
Apolisi yaying'ono ya Nkhamenya atamva za nkhaniyi adatengera mtsikanayu ku chipatala kuti akamuyeze, ndipo zotsatira za chipatala zidaonetsa kuti mtsikanayu adagonedwadi
Female
m'boma la Kasungu, akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wogwilira
m'boma la Kasungu, akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wogwilira
Female
Mmodzi wa ma agent a osewera mpira mkhalapakati wa osewera ndi matimu wati pokhapokha matimu ambiri m’dziko muno asiye kudana ndi ma agent
Mmodzi wa ma ejenti a osewera mpira mkhalapakati wa osewera ndi matimu wati pokhapokha matimu ambiri m’dziko muno asiye kudana ndi ma ejenti
Female
komanso kusowa upangiri wa oyimilira osewera ku matimu kukamapitilira, mpira sungatukuke ku Malawi kuno Onerani pologalamu ya Mtedza Mtedza madzulo ano nthawi ya 9:00 kuti mumve zambiri
komanso kusowa upangiri wa oyimilira osewera ku matimu kukamapitilira, mpira sungatukuke ku Malawi kuno Onerani pologalamu ya Mtedza Mtedza madzulo ano nthawi ya naini koloko kuti mumve zambiri
Female
Amayi ochuluka ochokera pansi pa ma T/A atatu a m'boma la Chikwawa ati asiya kumwa komanso kugwiritsa ntchito madzi kuchokera m'mitsinje ndi m'zithaphwi tsopano
Amayi ochuluka ochokera pansi pa ma Ti-e atatu a m'boma la Chikwawa ati asiya kumwa komanso kugwiritsa ntchito madzi kuchokera m'mitsinje ndi m'zithaphwi tsopano
Female
kutsatira kukumbidwa kwa Mijigo isanu ndi inayi imene Embassy ya dziko la Japan yapereka kudzera ku Gift of the givers Mkulu wa bungwe la Gift of the Givers a Sheriffa Mia
kutsatira kukumbidwa kwa Mijigo isanu ndi inayi imene Embase ya dziko la Japani yapereka kudzera ku Gifiti ofu ve givazi, Mkulu wa bungwe la Gifiti ofu ve givazi a Sherifa Miya
Female
wati bungwe lawo laboola mijigo isanu kwa Ngabu, iwiri kwa T/A Katunga komanso ina iwiri kwa T/A Maseya ndi cholinga chopereka madzi aukhondo
wati bungwe lawo laboola mijigo isanu kwa Ngabu, iwiri kwa Ti-e Katunga komanso ina iwiri kwa Ti-e Maseya ndi cholinga chopereka madzi aukhondo
Female
Wachiwiri kwa Kazembe wa dziko la Japan kuno ku Malawi a Seiji Tashiro anati mijigoyi ndi mphatso yochokera kwa mabungwe a Itochu Corporation
Wachiwiri kwa Kazembe wa dziko la Japani kuno ku Malawi a Seiji Tashiro anati mijigoyi ndi mphatso yochokera kwa mabungwe a Itochu kopaleshoni
Female
komanso Takemoto Oil ochokera ku Japan amene amagula chitowe kuchokera kwa alimi a m'boma la Chikwawa
komanso Takemoto Oyilo ochokera ku Japani amene amagula chitowe kuchokera kwa alimi a m'boma la Chikwawa
Female
Apolisi amanga a polisi anzawo awiri, omwe amagwira ntchito ku polisi ya Karonga
Apolisi amanga a polisi anzawo awiri, omwe amagwira ntchito ku polisi ya Karonga
Female
powaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhani yolowetsa mowa komanso lamya za mmanja mu chitokosi cha apolisi m'bomali
powaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhani yolowetsa mowa komanso lamya za mmanja mu chitokosi cha apolisi m'bomali
Female
Kumangidwa kwa apolisiwa kukudza pomwe kanema ina inafala pa masamba a mchezo imene imaonetsa anthu omwe akuwaganizira milandu yosiyanasiyana akumwa mowa koma ali m'chitokosi
Kumangidwa kwa apolisiwa kukudza pomwe kanema ina inafala pa masamba a mchezo imene imaonetsa anthu omwe akuwaganizira milandu yosiyanasiyana akumwa mowa koma ali m'chitokosi
Female
Malingana ndi mneneri wa polisi m'dziko muno a Peter Kalaya, apolisi amangidwawa ndi Sub Inspector Kaston Matemba
Malingana ndi mneneri wa polisi m'dziko muno a Pita Kalaya, apolisi amangidwawa ndi Sabu insipekita Kasitoni Matemba
Female
ndi Constable Brighton Mpombeza omwe akayankhe mlandu wa kulephera kusunga mwambo wa apolisi komanso kusagwiritsa bwino ntchito udindo wawo
ndi Konsitabo Bulayitoni Mpombeza omwe akayankhe mlandu wa kulephera kusunga mwambo wa apolisi komanso kusagwiritsa bwino ntchito udindo wawo
Female
Oganiziridwa apita nawo kubwalo la milandu posachedwapa
Oganiziridwa apita nawo kubwalo la milandu posachedwapa
Female
Bungwe la PAK foundation latenga ana awiri omwe amazisamalira okha kaamba koti makolo awo anamwalira zaka zinayi zapitazo, kuti liziwasamalira
Bungwe la PAKI faundeshoni latenga ana awiri omwe amazisamalira okha kaamba koti makolo awo anamwalira zaka zinayi zapitazo, kuti liziwasamalira
Female
Poyakhula ndi Times 360 Malawi, mkulu wa bungweli a Patricia Kaliati, ati akufuna akawaphunzitse anawa, amene ndi ochokera kwa mfumu yayikulu Juma m'boma la Mulanje, mpaka akatsirize maphunziro awo
Poyakhula ndi Taimusi filii sikisite Malawi, mkulu wa bungweli a Patilisha Kaliyati, ati akufuna akawaphunzitse anawa, amene ndi ochokera kwa mfumu yayikulu Juma m'boma la Mulanje, mpaka akatsirize maphunziro awo
Female
M'midzimu muli ana ambiri omwe ali ndi chidwi chofuna kuphunzira koma kaamba kochepekedwa ambiri sakumapitiriza maphunziro awo
M'midzimu muli ana ambiri omwe ali ndi chidwi chofuna kuphunzira koma kaamba kochepekedwa ambiri sakumapitiriza maphunziro awo
Female
ndiye ine kudzera ku bungwe langa ndikufuna ndikwanirise masomphenya a anawa, a Kaliati anafotokoza
ndiye ine kudzera ku bungwe langa ndikufuna ndikwanirise masomphenya a anawa, a Kaliati anafotokoza
Female
Kodi a Thomson Mpinganjira aziphunzitsa okha Wanderers? Okoma atani? Mighty Mukuru Wanderers ikusaka mphunzitsi watsopano kutsatira kuchoka kwa a Mark Harrison amene adamaliza chaka chatha opanda chikho
Kodi a Thomusoni Mpinganjira aziphunzitsa okha Wandilazi? Okoma atani? Maite Mukuru Wandilazi ikusaka mphunzitsi watsopano kutsatira kuchoka kwa a Maki Harisoni amene adamaliza chaka chatha opanda chikho
Female
Wanderers ndi imodzi mwa ma timu amene ali ndi ndalama zambiri komanso amene amatumiza osewera ambiri ku timu ya dziko lino ya Flames. Bvuto lingakhale chani
Wandilazi ndi imodzi mwa ma timu amene ali ndi ndalama zambiri komanso amene amatumiza osewera ambiri ku timu ya dziko lino ya Fulemuzi. Bvuto lingakhale chani
Female
Kodi Wanderers ikufunika mphunzitsi otani, Mu chaka cha 2022 Wanderers isadakatenge chikho cha Airtel Top 8
Kodi Wandilazi ikufunika mphunzitsi otani, Mu chaka cha twente twente thu Wandilazi isadakatenge chikho cha Eyatelo Topu eiti
Female
pogonjetsa FCB Nyasa Big Bullets, a Mpinganjira adayankhula ndi osewera a timuyi powalimbikitsa
pogonjetsa Efu sibi Nyasa Bigi Buletsi, a Mpinganjira adayankhula ndi osewera a timuyi powalimbikitsa
Female
Mphatso Malidadi anali nawo pa mwambowu ku Wanderers Club House kumene a Mpinganjira adayankhula motero
Mphatso Malidadi anali nawo pa mwambowu ku wandilazi kalabu hausi kumene a Mpinganjira adayankhula motero
Female
Bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula katundu m'dziko muno la Cama lapempha boma kuti likonze misewu, pomwe bungweri likuti misewu yambiri m'dziko muno siiri bwino
Bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula katundu m'dziko muno la kama lapempha boma kuti likonze misewu, pomwe bungweri likuti misewu yambiri m'dziko muno siiri bwino
Female
Kudzera mu kalata imene wasaina ndi mkulu wa bungweri a John Kapito, bungweri lati likudabwa kuti misewu yambiri m'dziko muno siiri bwino ngakhale akuti anthu ogula amadula msonkho
Kudzera mu kalata imene wasaina ndi mkulu wa bungweri a Joni Kapito, bungweri lati likudabwa kuti misewu yambiri m'dziko muno siiri bwino ngakhale akuti anthu ogula amadula msonkho
Female
komanso kulipra ndalama kudzera m'zipata za m'misewu komanso zomwe khonsolo za m'mizinda zimatolera, mwa zina
komanso kulipra ndalama kudzera m'zipata za m'misewu komanso zomwe khonsolo za m'mizinda zimatolera, mwa zina
Female
Iwo ati kuonongeka kwa misewu kukukhudza kwambiri anthu ogula kaamba koti akuononga ndalama zambiri
Iwo ati kuonongeka kwa misewu kukukhudza kwambiri anthu ogula kaamba koti akuononga ndalama zambiri
Female
pokonzetsa galimoto zawo zimene zimafunika ndalama zambiri kuti agule zipangizo zake m'maiko ena
pokonzetsa galimoto zawo zimene zimafunika ndalama zambiri kuti agule zipangizo zake m'maiko ena
Female
Iwo atsindika kufunika koti unduna woona za mtengatenga komanso nthambi ya Roads Authority, Roads Fund komanso khonsolo za m'mizinda ya dziko lino akonze vutoli mwachangu
Iwo atsindika kufunika koti unduna woona za mtengatenga komanso nthambi ya lodzi ofolite, lodzi fandi komanso khonsolo za m'mizinda ya dziko lino akonze vutoli mwachangu
Female
komanso kufotokozera dziko lino chifukwa chimene alolera kuti misewu ionongeke chotere
komanso kufotokozera dziko lino chifukwa chimene alolera kuti misewu ionongeke chotere
Nduna yoona za mtengatenga a Jacob Hara yati ndalama zimene boma limatolera pa mafuta komanso m'zipata za m'misewu sizikhala zokwanira
Nduna yoona za mtengatenga a Jakobo Hara yati ndalama zimene boma limatolera pa mafuta komanso m'zipata za m'misewu sizikhala zokwanira
Female
kuti likwanitse kukonza misewu imene ili yoonongeka
kuti likwanitse kukonza misewu imene ili yoonongeka
Female
Komabe a Hara ati Amalawi ayembekezere kuti zinthu zisintha kaamba koti posachedwapa boma likhazikitsa ntchito yokonzanso misewu yoonongeka
Komabe a Hara ati Amalawi ayembekezere kuti zinthu zisintha kaamba koti posachedwapa boma likhazikitsa ntchito yokonzanso misewu yoonongeka
Female
Ku Liberia, mwambo wolumbiritsa mtsogoleli watsopano wa dzikolo a Joseph Boakai unavutirapo, mtsogoleriyu atalephera kumaliza kuyankhula pa mwambowu, chifukwa chobanika kamba ka kutentha
Ku Laiberiya, mwambo wolumbiritsa mtsogoleli watsopano wa dzikolo a Jozefe Bowakai unavutirapo, mtsogoleriyu atalephera kumaliza kuyankhula pa mwambowu, chifukwa chobanika kamba ka kutentha
Female
A Boakai, omwe ndi a zaka 79 zakubadwa, anabanika atayamba kuyankhula kamba ka kutentha komwe akuti kunafika pa 30 degrees Celsius m'dzikolo
A Bowakayi, omwe ndi a zaka sevente naini zakubadwa, anabanika atayamba kuyankhula kamba ka kutentha komwe akuti kunafika pa fete digilizi seshazi m'dzikolo
Female
Iwo anapambana pa chisankho cha chibwereza chomwe amapikisana ndi mtsogoleri wakale wa dzikolo a George Weah
Iwo anapambana pa chisankho cha chibwereza chomwe amapikisana ndi mtsogoleri wakale wa dzikolo a Joji weya
Female
Poyankhula atapeza mtendere, asilikali atawakupiza ndi mapepala, a Boakai anati ali bwino kwambiri ndipo anthu m'dzikomo asade nkhawa
Poyankhula atapeza mtendere, asilikali atawakupiza ndi mapepala, a Bowakayi anati ali bwino kwambiri ndipo anthu m'dzikomo asade nkhawa
Female
ponena kuti ‘akulu akulu ndi m’dambo mozimira moto
ponena kuti ‘akulu akulu ndi m’dambo mozimira moto
Female
Atsikana ndi anyamata okwana makumi awiri ndi mphambu zitatu a m'dziko la South Africa ali mu nyumba momwe akhale kwa kanthawi mu mpikisano uja wa Big Brother Mzansi
Atsikana ndi anyamata okwana makumi awiri ndi mphambu zitatu a m'dziko la Saufi afilika ali mu nyumba momwe akhale kwa kanthawi mu mpikisano uja wa Bigi bulava Mzansi
Female
Big Brother Mzansi, yomwe ikuwonetsedwa pa DStv, yayamba Lamulungu Wopambana akuyembekezeka kulandira ndalama zankhaninkhani
Bigi bulava Mzansi, yomwe ikuwonetsedwa pa Diyesitivi, yayamba Lamulungu, Wopambana akuyembekezeka kulandira ndalama zankhaninkhani
Female
Mu nyumbamu, atsikana ndi anyamatawa amakhala akuchita masewero osiyanasiyana, Zaka za m'mbuyomu, mu mpikisanowu, umene unkadziwika kuti Big Brother Africa
Mu nyumbamu, atsikana ndi anyamatawa amakhala akuchita masewero osiyanasiyana, Zaka za m'mbuyomu, mu mpikisanowu, umene unkadziwika kuti Bigi bulava afilika
Female
munkakhalanso anthu a m'maiko ena a mu Africa, ndipo dziko la Malawi lakhala likutumiza nthumwi zake Mu nyumbamu, atsikana ndi anyamata wochita ntchito zosiyasiyana
munkakhalanso anthu a m'maiko ena a mu Afilika, ndipo dziko la Malawi lakhala likutumiza nthumwi zake Mu nyumbamu, atsikana ndi anyamata wochita ntchito zosiyasiyana
Female
womwe mu chingerezi amawatcha kuti 'housemates', amakhala limodzi ndi kuchitira masewero osiyanasiyana limodzi ndipo mwa zina, ena amatha kugwa m'chikondi
womwe mu chingerezi amawatcha kuti 'hausi metsi', amakhala limodzi ndi kuchitira masewero osiyanasiyana limodzi ndipo mwa zina, ena amatha kugwa m'chikondi
Female
Anthu a m'dera la mfumu yayikulu Nkanda boma la Mulanje akuyembekezera kuyamba kulandira thandizo labwino la chipatala, kutsatira kutsegulidwa kwa chipatala cha Othakarhaka foundation m'deralo
Anthu a m'dera la mfumu yayikulu Nkanda boma la Mulanje akuyembekezera kuyamba kulandira thandizo labwino la chipatala, kutsatira kutsegulidwa kwa chipatala cha Ofakalaka faundeshoni m'deralo
Female
M'modzi wa anthu ochokera m'deralo a Jessica Chikomola wati ngakhale ali ndi chipatala cha boma pafupi
M'modzi wa anthu ochokera m'deralo a Jesika Chikomola wati ngakhale ali ndi chipatala cha boma pafupi
Female
nthawi zambiri anthu samalandira mankhwala ndipo pena amangolemberedwa mankhwala n'kuuzidwa kuti akagule m'malo ogulitsa mankhwala
nthawi zambiri anthu samalandira mankhwala ndipo pena amangolemberedwa mankhwala n'kuuzidwa kuti akagule m'malo ogulitsa mankhwala
Female
Tiyamikire akuluakulu abungwe limeneli potiganizira kutsegula chipatala chomwe chithandizire kuteteza miyoyo ya anthu ochuluka m'dera lino, anatero a Chikomola
Tiyamikire akuluakulu abungwe limeneli potiganizira kutsegula chipatala chomwe chithandizire kuteteza miyoyo ya anthu ochuluka m'dera lino, anatero a Chikomola
Female
Mkulu wa bungweli a Ida Puliwa Mwango, wati chipatalachi chikhala ndi mbali ziwiri, yolipira komanso yaulere ndi cholinga choti ndalama zomwe azipeza mbali yolipira
Mkulu wa bungweli a Ida Puliwa Mwango, wati chipatalachi chikhala ndi mbali ziwiri, yolipira komanso yaulere ndi cholinga choti ndalama zomwe azipeza mbali yolipira
Female
azithandizira kugulira mankhwala komanso kulipilira ana amasiye ndi ovutika omwe bungweli limawathandiza
azithandizira kugulira mankhwala komanso kulipilira ana amasiye ndi ovutika omwe bungweli limawathandiza
Female
Iwo apempha anthu kuti azipita ku chipatalachi kukapeza thandizo la chipatala ngati njira imodzi yothandiza pothana ndi mavuto omwe anthu amakumana nawo m'bomalo
Iwo apempha anthu kuti azipita ku chipatalachi kukapeza thandizo la chipatala ngati njira imodzi yothandiza pothana ndi mavuto omwe anthu amakumana nawo m'bomalo
Female
Kupatula kuthandiza pa ntchito za umoyo, bungweli limagwira ntchito ya zaulimi, maphunziro komanso kusamalira zachilengedwe
Kupatula kuthandiza pa ntchito za umoyo, bungweli limagwira ntchito ya zaulimi, maphunziro komanso kusamalira zachilengedwe
Female
Wapampando wa khonsolo ya boma la Nkhotakota khansala Charles Chimzukuzuku wapempha anthu m'bomali kuti ayike chidwi choteteza ndi kusamalira mitengo yomwe ikubzalidwa m'bomali
Wapampando wa khonsolo ya boma la Nkhotakota khansala Tchalosi Chimzukuzuku wapempha anthu m'bomali kuti ayike chidwi choteteza ndi kusamalira mitengo yomwe ikubzalidwa m'bomali
Female
Iwo ati, ndi zodandaulisa kuti mitengo imabzalidwa chaka ndi chaka m'bomali koma mitengo yomwe imakula ndi yochepa
Iwo ati, ndi zodandaulisa kuti mitengo imabzalidwa chaka ndi chaka m'bomali koma mitengo yomwe imakula ndi yochepa
Female
Khansalayu wapereka pempholi pa mwambo wokhazikitsa ntchito yobzala mitengo ya chaka chino pasukulu ya pulayimale ya Dzikondilonse m'boma la m'mbali mwa nyanjali
Khansalayu wapereka pempholi pa mwambo wokhazikitsa ntchito yobzala mitengo ya chaka chino pasukulu ya pulayimale ya Dzikondilonse m'boma la m'mbali mwa nyanjali
Female
Nkhonsoloyi yaika chiwerengero cha mitengo yosachepera 1.3 million yomwe ikufuna kubzala munyengoyi m'bomali
Nkhonsoloyi yaika chiwerengero cha mitengo yosachepera wani pointi fili miliyoni yomwe ikufuna kubzala munyengoyi m'bomali
Female
Bwalo la First grade magistrate ku Neno lagamula bambo wa zaka 61 a Bertno Mpapa kukakhala ku ndende ndi kukagwira ukaidi wopanda kalavulagaga kwa zaka 10
Bwalo la Fesiti giledi majesitileti ku Neno lagamula bambo wa zaka sikisite wani a Betino Mpapa kukakhala ku ndende ndi kukagwira ukaidi wopanda kalavulagaga kwa zaka teni
Female
atawapeza olakwa pa mlandu wogona ndi mwana zaka 16 yemwe amamusunga kunyumba kwawo Bwaloli lidamva kuti a Mpapa adapalamula mlanduwu m'mwezi wa June chaka chatha
atawapeza olakwa pa mlandu wogona ndi mwana zaka sikisitini yemwe amamusunga kunyumba kwawo Bwaloli lidamva kuti a Mpapa adapalamula mlanduwu m'mwezi wa Juni chaka chatha
Female
ndipo ataonekera ku bwalo la milandu kangapo, adaukana mlanduwu pambali pa mboni zomwe bwaloli lidabweretsa
ndipo ataonekera ku bwalo la milandu kangapo, adaukana mlanduwu pambali pa mboni zomwe bwaloli lidabweretsa
Female
Lero ,Lachiwiri a Mpapa adaonekeraso kubwaloli, lomwe lawapeza olakwa pa mlanduwu ndipo bwaloli lati lapereka chigamulochi potengeranso zaka za opalamulawa
Lero ,Lachiwiri a Mpapa adaonekeraso kubwaloli, lomwe lawapeza olakwa pa mlanduwu ndipo bwaloli lati lapereka chigamulochi potengeranso zaka za opalamulawa
Female
A Mpapa amachokera m'mudzi mwa Donda mfumu yaikulu Chekucheku m'boma lomweli la Neno
A Mpapa amachokera m'mudzi mwa Donda mfumu yaikulu Chekucheku m'boma lomweli la Neno
Female
Akonzi a kanema ya School Days ati akulimbikitsika kwambiri kuti apitirize kupanga makanema ambiri komanso othyakuka malingana ndi mmene anthu akuwalimbikitsira
Akonzi a kanema ya sukulu dwyizi ati akulimbikitsika kwambiri kuti apitirize kupanga makanema ambiri komanso othyakuka malingana ndi mmene anthu akuwalimbikitsira
Female
Anthu okwana 1 million aonera kale kanemayu, yemwe akutambasula kwambiri za nkhani za moyo wa ku sukulu ya sekondale, mu sabata zitatu chiyiyikileni pa tsamba la mchezo la YouTube
Anthu okwana wani miliyini aonera kale kanemayu, yemwe akutambasula kwambiri za nkhani za moyo wa ku sukulu ya sekondale, mu sabata zitatu chiyiyikileni pa tsamba la mchezo la Yuchubu
Female
Anthu akutipatsa mangolomera ndipo tikufuna tichite zambiri", watero mmodzi mwa akonzi, Kendall Kamwendo yemwenso amayimba
Anthu akutipatsa mangolomera ndipo tikufuna tichite zambiri", watero mmodzi mwa akonzi, Kendo Kamwendo yemwenso amayimba
Female
Kanemayu amuonetsa mu mzinda wa Blantyre ku hotela ya Amaryllis Loweruka likudzali, ndipo anthu adzakhalanso ndi mwayi wocheza ndi akatswiri omwe ali mukanemayu
Female Kanemayu amuonetsa mu mzinda wa Bulantaya ku hotela ya Amalezi Loweruka likudzali, ndipo anthu adzakhalanso ndi mwayi wocheza ndi akatswiri omwe ali mukanemayu
Female
yemwe anatenga gawo la wophunzira wa folomu folo, yemwe adali wovuta, ndipo amadziwika ndi dzina loti Phwedo
yemwe anatenga gawo la wophunzira wa folomu folo, yemwe adali wovuta, ndipo amadziwika ndi dzina loti Phwedo
Female
Wosewera mpira wamiyendo wakale wa Flames ndi FCB Nyasa Big Bullets, Fischer Kondowe
Wosewera mpira wamiyendo wakale wa Fulemuzi ndi Efusi bi Nyasa Bigi Buletsi, Fisha Kondowe
Female
komanso angathe kupikisana ndikuposa ena amasiku ano chifukwa ambiri samadziyang'anira bwino Jahman kapena kuti Fischer anacheza ndi Mphatso Malidadi motere
komanso angathe kupikisana ndikuposa ena amasiku ano chifukwa ambiri samadziyang'anira bwino Jamani kapena kuti Fisha anacheza ndi Mphatso Malidadi motere
Female
Madzi osefukira awononga minda ya alimi ochuluka m'madera a mafumu Malengachanzi ndi Mphonde m'boma la Nkhotakota
Madzi osefukira awononga minda ya alimi ochuluka m'madera a mafumu Malengachanzi ndi Mphonde m'boma la Nkhotakota
Female
Madziwa, omwe adza kamba ka mvula yamphamvu yomwe yagwa kwa masiku awiri m'bomali
Madziwa, omwe adza kamba ka mvula yamphamvu yomwe yagwa kwa masiku awiri m'bomali
Female
achititsa kuti mtsinje wa Kaombe m'bomali udzadze ndi kusefikira ndi kuononga mbewu m'minda yozungulira mtsinjewu m'maderawa
achititsa kuti mtsinje wa Kaombe m'bomali udzadze ndi kusefikira ndi kuononga mbewu m'minda yozungulira mtsinjewu m'maderawa
Female
M'modzi wa anthu okhudzidwa ndi ngoziyi a Itheithe Major wati madziwa akhudza minda yomwe ili pa mtunda wa mamita 400 kuchoka pa mtsinjewu
M'modzi wa anthu okhudzidwa ndi ngoziyi a Itheithe Meja wati madziwa akhudza minda yomwe ili pa mtunda wa mamita folohandede kuchoka pa mtsinjewu
Female
Yemwe akugwirizira udindo wa mkulu wa ofesi yowona zangozi zogwa mwadzidzidzi m'bomali a George Zibophe wati adayendera malowa
Yemwe akugwirizira udindo wa mkulu wa ofesi yowona zangozi zogwa mwadzidzidzi m'bomali a Joji Zibophe wati adayendera malowa
Female
ndipo pakadali pano akuunguza kuchuluka kwa minda yomwe yakhudziwa ndi ngoziyi
ndipo pakadali pano akuunguza kuchuluka kwa minda yomwe yakhudziwa ndi ngoziyi
Female
Mwana amene ali m'chithunzichi, m'manja mwa mayi ake, ndi Rejoice Frankson, wa miyezi 11 yakubadwa. Iye ali pa chiopsezo chachikulu kaamba ka vuto la kubooka kwa mtima
Mwana amene ali m'chithunzichi, m'manja mwa mayi ake, ndi Lijoisi Fulankisoni, wa miyezi leveni yakubadwa. Iye ali pa chiopsezo chachikulu kaamba ka vuto la kubooka kwa mtima
Female
Poyankhula ndi Times 360 Malawi, mayi akewa, aTesha Patheletu, ati mwanayu
Poyankhula ndi Taimusi fili sikisite Malawi, mayi akewa, aTesha Patheletu, ati mwanayu
Female
akhala akuyenda naye m'zipatala zosiyanasiyana kufikira pamene chipatala chachikulu cha Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe chidapeza vutoli
akhala akuyenda naye m'zipatala zosiyanasiyana kufikira pamene chipatala chachikulu cha Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe chidapeza vutoli
Female
M'mawu awo, a Patheletu ati pakadali pano chimene chikusowekera ndi ndalama zopangitsira chiphaso choyendera
M'mawu awo, a Patheletu ati pakadali pano chimene chikusowekera ndi ndalama zopangitsira chiphaso choyendera
Female
komanso ndalama zodyela pamene boma likuwatumiza ku chipatala cha dziko la India kuti akalandire thandizo
komanso ndalama zodyela pamene boma likuwatumiza ku chipatala cha dziko la Indiya kuti akalandire thandizo
Female
Ndikupempha kwa anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino kuti andithandize chifukwa banja langa ndi losauka, kotero sitingakwanitse kupeza ndalama zopangitsira passport
Ndikupempha kwa anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino kuti andithandize chifukwa banja langa ndi losauka, kotero sitingakwanitse kupeza ndalama zopangitsira pasipoti
Female
komanso zodyera pa ulendo wopita ku India kuti tikalandire thandizo la mwanayu, atero a Patheletu
komanso zodyera pa ulendo wopita ku India kuti tikalandire thandizo la mwanayu, atero a Patheletu
Female
Ndipo mneneri wa chipatala cha Kamuzu central mu mzinda wa Lilongwe a Winnie Yotamu watsindika za vuto la mwanayu
Ndipo mneneri wa chipatala cha Kamuzu sentilo mu mzinda wa Lilongwe a Wini Yotamu watsindika za vuto la mwanayu
Female
Amene akufuna kumva zambiri komanso kuthandiza atha kuimba lamya pa nambala izi: Apolisi ku Lilongwe amanga anthu 7
Amene akufuna kumva zambiri komanso kuthandiza atha kuimba lamya pa nambala izi: Apolisi ku Lilongwe amanga anthu seveni
Female
komanso kupeza njinga zamoto 12 zomwe zinabedwa m'mwezi wa December ku Area 4 mu mzindawo
komanso kupeza njinga zamoto twelofu zomwe zinabedwa m'mwezi wa Disemba ku Area folo mu mzindawo
Female
Mneneri wa Polisi a Hastings Chigalu wati anthuwa akuganiziridwa kuti adathyola malo osungira katundu a nzika ya dziko la China
Mneneri wa Polisi a Hesiting’izi Chigalu wati anthuwa akuganiziridwa kuti adathyola malo osungira katundu a nzika ya dziko la Tchaina
Female